Makhonzedwe a Nsomba Nsomba zasiwisi sizingasungidwe nthawi yayitali osayika mufiliji, ndiye tiyenera kuzikhonza nsombazo kuti zitetezedwe kuti zisaole. Ogulitsa nsomba ambiri akugwira ntchito m'mphepete mwanyanja. Amagula nsomba kuchokera kwa asodzi ndikuwamba ndikunyamula kukagulitsa kunsika kutauni. Ukamawamba nsomba, munthu umafunika kukhala ndizipangizo zofunikira ndi ndalama. Pali midzi yambili imene imawamba nsomba mumphepete mwanyanja, kumene anthu amakhala pamodzi kugula ndikuwamba nsomba. Kodi nsomba timaziwambiranji? Pali njira zambiri zakawambidwe kansomba, makamaka ndi mtundu wake wansombazo. Njira zosiyanasiyana zakawambidwe kansomba zimapangitsanso kuti nsomba zikome mosiyanasiyana. |
![]() Kuyanika nsomba pa thandara |
![]() Kuyanika Utaka pa thandara |
1) Nsomba Zouma Kuyanika nsomba pa dzuwa ndi njira imodzi yokondedwa yakawambidwe kansomba zazing'onozing'ono monga ngati Utaka, Usipa, Matemba ndi Micheni yaying'onoying'ono. Kuti munthu uyanike nsomba umafunika kuziyika pachithandala ndikumadzitembenuza kamodzi kapena kawiri patsiku kuti ziume bwino mbali zonse ziwiri. Kuyanika nsomba kuti ziume bwinobwino kumatenga masiku atatu kapena anayi, ndipo nsomba zichotsedwe pachithandala usiku uli wonse kapena ngati kuli mvula kuti zisanyowe. |
2) Nsomba Zofwafwaza Usipa okha ndiumene umakonzedwa mwanjira imeneyi. Usipa umaphikidwa kaye ndipo kenako umayanikidwa pachithandara kuti uwume ndi dzuwa. Usipa kuti ufike powuma bwino ndi dzuwa, umatenga masiku awiri kapena atatu ndipo kukoma kwake ndikosiyana ndiusipa wowumitsidwa mwanjira ina. |
![]() Kuwilitsa Usipa |
3) Nsomba Zootcha Nsomba monga Utaka, Mayani ndi Chendamwamba ndizimene zimawambidwa mwanjira imeneyi. Poyamba nsomba zimayanikidwa pa ma ola ochepa kenako zimaotchedwa pachilata mbali zonse dziwiri. Kenako nsomba zimayikidwa pachithandara kuti ziume tsiku lonse. Kakonzendwe aka kamatenga tsiku limodzi kapena awiri ndipo kukoma kwake kumasiyana ndikakonzedwe kena kansomba. |
![]() Kuotcha Utaka pa moto |
![]() Kuyika Nsomba pa waya |
4) Nsomba Zowamba Kuwamba nsomba pamoto ndi njira yokhayo imene imagwiritsidwa pokhonza nsomba monga ngati Chambo, Kampango, Milamba ndi Micheni yayikuluyikulu. Nsomba zazing'onozing'ono nazonso zimawambidwa pamoto chifukwa chakakomedwe kake ndikutinso zimawambidwa mukanthawi kochepa. |
Nsomba zimayanikidwa kum'mawa kapena kumazulo kokha, kenako zimayikidwa pachiwaya mubayara usiku wonse. Nsomba zazikulu ngati Kampango, Chambo kapena Milamba zimayamba kung'ambidwa ndikutsukidwa zisanawambidwe. Kuwamba pamoto kumagwilitsidwa ntchito kwambiri nthawi yamvula chifukwa kuotcha sikumasokonezeka ndi mvula. |
![]() Kuyatsa moto mubayara |
![]() Nkhalango yowonongeka ku Mareli Island |
Kuwamba Nsomba Ndikasamalidwe ka Nkhalango
Kuyerekezera ndi kawambidwe kena kansomba, kuwamba nsomba pamoto kumafuna nkhuni zambiri. Kuti moto wowambira nsomba ukhale ukukolera usiku wonse ndiye kuti pangafunike nkhuni zophikira mulungu umodzi wathunthu. Ndiye nkhalango iyenera kusamalilidwa bwino pa kubyala mitengo yoti yikule, kupanda apo mitengo itha yonse pasachedwapa ndipo nkhalango izakhala chipululu. |